1Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.” Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu; onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.
2Imvani pemphero langa, Inu Mulungu mvetserani mawu a pakamwa panga.
3Alendo akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga, anthu amene salabadira za Mulungu.
4Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa; Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.
5Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe; mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.
6Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu; ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova, pakuti ndi labwino.
7Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse, ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.